Mibvumbi ya madalitso
1. Mivumbi ya madalitso. ili ndi lonjezano.
Pazadza nyengo ya mvula. yotumidwa ndi Mbuye.
CHORUS:
Mivunbi ndiyo, ya madalitso idze
Madontho akugwa koma mivumbyo itsike.
2. Mivumbi ya madalitso yotitsitsimutsanso,
Pa mapiri madambo. pamvekedwe mvulayo.
3. Mivumbi ya madalitso. Mutitumizereni.
Mbuya tipatseni mdzutso. Mawu mukwaniritse.
4. Mivumbi ya madalitso, bwenzi itatigwera.
Kwa Mulungu tivomereza, kwa Yesu tiitana.
5. Mivumbi ya madalitso, ngati timvera lye.
Mvula Itsanuliridwa, monga kufuna kwake.