Ndidze Pafupipa

 


1. Ndidze pafupi pa Mlungu wanga,
Ngakhale pamtanda Mundikweza;
Koma ndiimbabe, Mbuye mndikhalitse,
Mbuye mndikhalitse
M’fupi Ndinu.


2. Ngakhale kuthengo Ndasokera,
M’mdima ndigonapa E, pamwala;
Koma m’kulotako Ndiyandikizanso
Ndiyandikizanso
M’fupi Ndinu.


3. Pajapo ndipenya Pokwerapo,
Angelo atsika Kumwambako,
Ndiwo akodola Kuti ndikabwere,
Kuti ndikabwere,
M’fupi Ndinu.


4. Tsono poukanso Wokondwatu,
Ndipeza pomwepo Pali Mlungu;
Ndipo masautso Andisendezanso,
Andisendezanso,
M’fupi Ndinu.


5. Pena pakufadi, N’kweza m’Mwamba,
DZuwa ndi nyenyezu Zitsalira;
Pomwe ndiimbanso, Ndidza pafupi pa,
Ndidza pafupi pa
Mlungu wanga.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *