Msandipitilire Yesu

 


Msandipitilire, Yesu, mundimvere Ine;
Mulikudalitsa ena,
M’sandipitilire


Chorus
Yesu, Mbuye, khutu munditchere;
M’mene muitono eno,
Msandipitirire.


Ndigwadira Inu, Yesu, Musandikanize;
Ndikalapatu machimo,
Mbuye, m’ndithandize.


Nkhope yanu ndifunitsa, Sind’yenera konse;
M’mtima mwanga muchirirtse
Nthenda zanga zonse.


Yesu, ndinutu chitsime Cha chimwemwe chokha;
Sindifuna wina konse,
Koma inu nokha.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *