M’mawa Tizifesa

 


1. M’mawa tizifesa Mbewu zakukoma,
Msana ndi usiku Tizifesa momwe.
Nyengo yamasika Tidzatema m’munda
Tidzabwera tonse Ndi zipatsozo.


Ref
Ndi zipatsozo, Ndi zipatsozo,
Tidzabwera tonse Ndizipatsozo.


2. Tizifesa m’dzuwa, Tizifesa m’mthunzi,
Sitiopa ife Mtambo ndi chisanu.
Athatu masika Ntchitozi zidatha;
Tidzabwera tonse Ndi zipatsozo.


3. Tingolira kaya, Koma tidzafesa
Mbewu ya Ambuye; Ntchitoyo nja Yesu.
Adzachotsa msozi, Adzatilandira,
Tidzabwera tonse Ndi zipatsozo.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *