Bwenzi Lathu Ndiye Yesu

 


1.Bwenzi lathu ndiye Yesu, Atikonda ifetu,
Zifunsiro zathu zonse, Tipemphere Mbuyathu;
Mtima phe tisowa tonse, Zitibvuta cabeko,
Kaamba sitimanka konse Kumpemphera Mlunguyo.


2.Tiri nazo zotiyesa, Zitidetsa nkhawamu,
Tisadandaule cabe, Timpephere Mbuyathu;
Kodi tikaona wina, Timkhulupiramo?
Yesu atidziwa bwino, Timpemphere yekhayo.


3.Kodi titolema namo, Zotiwawa m’mitmamo,
Atipulumutsa Yesu, TImpempere Iyeyu.
Kodi atothawa ’bale, Pempheratu bwenzilo,
Akusunga mkono mwace, Udzapumuliramo.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *