Kwa Inu Yesu Ndilira
1. Kwa Inu Yesu ndilira,
Wopanda Inu ndidzafa;
Mupulumutse inedi,
Mundilandiretu.
Refrain
Mundilandiretu,
Ndiipa m’mtimao;
Kotero mnandiferatu,
Mundilandiretu.
2. Ndifoka ndi zoipazo,
Ndidzalatu ndi machismo,
Sinditha kuzitayazo;
Mundilandiretu.
3. Ndayesa kudzikonzadi,
Ndapeza mphamvu ndilibe,
Zoipa zakanikadi;
Mundilandiretu.
4. Onani Mbuye ndigonja,
Kuyesa kwanga ndaleka;
Chitani Inu mumtima;
Mundilandiretu.
5. Muyambe ntchito yanuyi,
Musalekenso, chitani;
Ndidzipereka leroli;
Mundilandiretu.